Bismillah Al-Rehman
Al-Raheem
Anti Ahmadiyya
Movement in Islam
MMENE YEMWE ANAYAMBA GURU
LA AHMADIYYA ANANYOZERA MTUMIKI MUHAMMAD (SAW)
OLEMBE
DR. SYED RASHID ALI.
Zonse zotamandidwa ndi za
Allah, umodzi yekha ndipo ndiyemweyo. Chikondi chake ndi madalitso yangagwele
mwamuya-ya-ya pa woyela Mtumiki Muhammad pambuyo pache palibe wina Mtumiki.
Anthu a kudziko ya Ulaya
(Britain) anatenga mwaupandu ula-mililo wa a muslim wa India sub-contient ndipo
lolemekezedwa linatumidwa kudziko la
India ku chokela ku nyumba ya malamulo la ku Ulaya kuti apeze njira
yomwe angaletse chikhulupililo cha Jihadi.
Pambuyo pa zaka ziwiri
zomafufuza, bungweri linapereka zofufuza zao
zomwe mutu wace unati “ Kufunika kuganizila kuti a musilamu abvomere
mutsogoreri wao wa ci Islam pa maso pao. Lero maganiza a zopeza munthu emwe a ngazipange ngati
mtumiki wansembe. Mirza Ghulam Ahmad anasankhidwa kuti a kwaniritse nchito
chifukwa chakuti anali wa mbado wa anthu a ku Ulaya, ndiponso makharidwe ake
ndi chikhulupiriro chace cha za Mulungu.
Anapeza mwa iye munthu
wocita zabwino. Patapita zaka, anabvomela mkalata yomwe analemba kwa olamurira
wamkulu wa Punjab kuti anangozipanga ku khala ngati Mtumiki wansembe mau awa apezeka mbukhu lache; kitab-ul-Bariyah.
Roohani Khazain vol. 13 p.350 kwa aliyense kuti aone. Mirza Ghulam anakhula
kapolo wa Islam, osinthitsa umoyo ndipo anakwela ndime zambiri ndi zomwe zinali
kuchedwa Mtumiki. Zikhalidwe zake zinapangitsa kuti apite pamwamba pa mipingo
yambiri. Kuyambira pa ukupolo wa Islam, wositha chikhulupililo cha
Islam-M’mahadith-Mujaddid- Oringana ndi Eisa ibne Maryam (mueneri
woronjezedwa)- Imam Mahdi-Mtumiki wotumidwa- Adam-Sari- Noah- Abraham- Isaac-
Ishmael- Joseph- David- Solomon- Jonas- Lord Krishna- Jai Singh Bahadwi, palibe
pomwe ankaimirira pothela pache, zikhulupiriro zace za bodza zinamukakamiza
kunena kuti anali woyela Mtumiki Muhammad
ndoponso kubwera kwachiwiri. Ndipo analemba : “ Uyo amene asiyamika ine
ndi Mustafa sanandione ndiponso sanandizindikile.”
(Roohani Khazain vol. P.259). Lero emwe anayamba ngati kapolo anakhala mfumu
mwa iye yekha.
Mirza Ghulam Ahmad
anakhazikisha guru la Ahmadiyya zaka zikwi-zikwi zapita kumbuyo uku
poyendeletsedwa ndi a British kufikira lero lino. Angakhale lero anthu amene
apezeka m’gururi aphatikiza aja omwe ali ndi mantha akubwelanso mu chiIslam. Onse azindikila kuti ngati m’Muslim
wachoka ndi kutsata Ahmadiyyah azachepetsa unyiji wa a Muslim. A Muslim
amaphunzilo osiyana-siyana ndi a maganizo oasiyana- siyana m’maiko onse ndi
ogwirizana muchikhulupiriro cao cha kuti Mirza Ghulam Ahmad anali ochimwa
osakhulupirira ndipo sanali m’njira
yachiIslam, ndiponso aliyense omtsatira, angakhali kuti ndi Qadiani,
Ahmadi wa ku Lahori, nayeso ndi wochoka mnjira ya chi Islam. Mu nkhani ya kutha kwa caka ca 1974, ophunzira mwakuya
pa za Mulungu analengeza kuti Mirza Ghulam Ahmad ndi onse omutsatira alibe chikhuhipiriro cha Islam.
Angakhale lero, kuonetsa
monga ali a Sunni Muslim ndipo kaswili wa Islam, guru la Ahmadiyyah ipitiriza
kunama anthu osaphunzila ndi osanka omwe ali, a Muslim m’balu zosiyana- siyana
za dziko. Zolemba zao ziimiliza mbali imodzi mwadala kuyopa zo khulupilira za
omwe anayamba gululi.
Mwa tsopano apa, pepala
linalembedwa ndi ku turutsidwa ndi guru la Ahmadiyyah/Qadianiyah mu mbari
zambiri za m’maiko “Ahmad muchitamando
cha zikhalidwe za Indo-Pakistan, maina monga Ghulam Ahmad, Ghulam Rasool
, Ghulam Ali Kapena Abdul Rahman ndi ena ndi maina opangidwa ndiponso
yatanthauza Ghulam (Kapolo) wa Ahmad, Kapolo wa Rasool, Kapolo wa Ali kapena
wanchito wa Rehman (wachifundo). Ndichodabwitsa ndiponso umene Ghulam Kapena
Kapolo wa Ahmed alamurira mfumu yake ?
Mpepalari mupezeka nkhani
zomwe zinalembedwa ndi yemwe anayamba gulu la Ahmadiyya, Mirza Ghulam Ahmad
Qadiani, kuyesa kuonetsa kuti anali ledzela ndi chikundi cha woyela Mtumiki Muhammad
(S.A.W), odzala ndi zithokoza za Allah, Qur’an loyela la Islam. Zomwe analemba
Ghulam simuonetsa munthu wabwino. Koma yamwe Ahmad anali ndi madela awiri
osiyana mu umoyo wace.
Dela loyamba linacokela ku
umwana wace kufika koyambila kwa ukulu wa umoyo wake. Popeza kuti anabadwa mu
banja la Muslim, pa nthawi anali wachikhulupiliro cha Sunni Muslim. Inali pa
nthawi imene pomwe ananenelera mobwezara za chikulupiliro cha Sunni Muslim.
Inali pa nthawi imeneyi pomwe ananenelera mobwezapo za chikhulipiliro cha
Muslim Ahle-Sunnah wal Jammat, ndi chikondi ca woyela Mtumiki wa Islam ndi
kufuna kwace kugwila nchito ya Islam. Angakhale kuti analandila maphunziko ache
atsopano ku sukulu (madrassah) la maphunziko a Mulungu kapena kuti anapeza ulangizi wa uzimu kulingana
ndi mwanabo koma anali kuzithandiza yekha kupanga ziganizo ndi ndakatulo. Ngati
kunali kucoka mnjira yokhazikitsidwa ya ahle Sunnah- Jamaat, ici sichinonekele.
Pambuyo pace, maganizo ndi
zikhulupililo zace zinaonetsa kusintha ndipo anaonetsa kucotsa nzeru kuzomwe
anali kunena ndi nthawi, anayambaso kucita zinthu zosayenera ndipo anaonetsa
kucotsa nzeru kuzomwe anali kunena ndi kulemba sosaenela a Muslim. Koma kupita
kwa nthawi, anayambaso kucita zinthu zosayenela. Ndipo iyi mbali yoipa ya Mirza
Ghulam Ahmad inabisidwa ku anthu ndipo sinalembedwe m’mabukhu ya Guru la
Ahmadiyya.
Mbali ina yomwe ifunika
ku kumbukira ndi zolemba za Mirza Ghulam
Ahmad momwe anabvomela kuti anali kudwala matenda osiyana siyana ya mubongo
yomwe anali ku sokoneza maganizo ace .
Akunena matenda monga a Machola, Minejaitisi, kuyiwala zinthu mwamsanga ,
khunyu, chizwezwe, kutaya madzi kawiri-kawiri. Anenanso matenda ena monga
unyomwa ndi kusowa mphamvu ya kumvana. Akunena zamankhwala ambiri omwe
ankazipangila ndipo ena omwe anali kutenga ku anthu. Akunenanso kumwa zinthu
monga mu wine kukhala ngati mankhwara. Anali kulota angelo omwe anali kumuuza
mtengo kapena mankhwala ambiri ya kuti amunthandize pakuonjeza mphamu za kumva
wace. Ndipo tsiku lina Mulungu anamuuza kuturo kuti akonze mankhwala ya kumwa
ndipo chimodzi chomwe chi nali kufunika kusakaniza mu mankhwala amenewa cinali
OPIUM.
Kodi analidi odzala ndi
chikundi cha Mtumiki oyela ? Kodi anali Mtumiki ? Kapena zinali nchito zace
bongo wodwala chifukwa ca kumwa OPIUM ndi mowa?
M’matsamba yokonkhapo,
ndizaonetsa zolembedwa zopezeka m’mabukhu yolembedwa ndi Mirza Ghulam Ahmad
kuti owelenga aganizile okha m’mene munthuyu anali. Chizakhala kuti imwe kupeza
colinga ca emwe anapeza guru la Ahmadiyyah.
MIRZA GHULAM AHMAD
NDI MULUNGU WACE
Mu zolembedwa zao a guru
la Ahmadiyya azionetsa za cikondi ca mtsogeleri wao ndi chithokhozo cha Allah.
Kulondora zilembedwe za m’mabukhu mwace zionetsa kuti Mirza Ghulam Ahmad WAHI
ndizo khumba zinamulengetsa iye kutenga njira ina.
“ Ndinaona m’maso mwanga
kuti ine ndine Mulungu ndikukhulugilira kuti umulungu unalowa mu thupi langa
ndipo ndinali kunena kuti tifuna m’mwamba ndi pansi. Ndipo ndinalenga m’mwamba
ndi pansi. (Roohani Khazain vol. 13 p.103).
Tsiku lina Hazrat Maseeh
Mowood anaulula momwe anali kumvelera. Anaulula izi cifukwa anali kuzimwera
wamphamvu zomwe zalengezedwa ndi Mulungu.
( Trust N° 34, Islam
Quarbani p.12 Qazi la Muhammad Qadiani, emwe anali mzace wa Mirza Ghulam).
(Subhan Allah! Kunama
Allah pa za uwelewele ! Tipemphe Allah aticinjilize pa maganizo otayisa otele).
“ (Mirza !) Kumwamba ndi
pansi kuli ndi iwe monga ku liri ndi ine. Ucokela kwa ine mchigwilizano
ndi kumva ine ndekha. Ucokela kwa ine
monga ufumu wanga. Ucoka mwa ine monga mwana
wanga…ndimalakwa ndipo ndimacita zomwe nalengeza…Ndimaima kudwa.
Tikupatsa ulemelero wa HAQ monga kuti Mulungu watsika kucoka kumwamba.
Tikupatsa ulema wa mwana.”
(Haqiqat-ul-Wahy, Roohani
Khazain vol. 22 p.79-99).
MIRZA GHULAM NDI
MTUMIKI WOYELA MUHAMMAD
Mabukhu olembedwa ndi guru
la Ahmadiyya ndilodzala ndi zolembedwa za Mirza zomwe zionetsa chikondi cha
Mtumiki woyela Muhammad (Sal-Allaho alaihi wa Sallam). Kulondola zolembedwazi
m’mabukuwa zionetsa nkhani yosiyana-siyana
Ghulam poyamba anali wa
nchito wa AHMAD (MUHAMMAD) pambayo pace analedzela ndi chikondi cake. Kuledzela
kumeneku kunaongonga umoyo wace ndipo anakhala Muhammad (SAW). Kodi amene
amtsatila (Qadianis/ Ahmadis/ Lahoris/ Mirzais) adziwa zolembedwazi ? Ngati ali oziziwa, kodi mnjira
anazibisa kuti zitsadziwike?
Mirza Anena kuti
ndi wa nchito (kapole) ndiponso ndi wa chikondi cha Mtumikiti woyela Muhammad
SAW.
Zolembezedwa mu kapepala komwe mutu wake ukuti, “Ahmadi
athokoza Muhammad,” Mirza akunena kuti ndi wodzela ndi chikondi cha Muhammad
(SAW).” Uyu odzicetsa yekha sali Mtumiki kapena otumidwa kupena kapolo
olondola.”
(Man a Mirza Ghulam Ahmad,
Akhbar Alhakum Qadian N° 23 vol. 5)
pambuyo pa Mulungu ndi
oledzela ndi chikondi cha Muhammad. Ngati uyu simusilamu, Mulungu wanga ndine
munthu usayenela.
(Zokambidwa za Mirza
mpepala : “Ahmad nichithokozo wa Muhammad, p.1).
atanetsa omutsatila ake za
chikondi wache cha Mtumiki woyela Muhammad (SAW), anapitiliza kuonetsa kuti,
chikondi cake casandutsa thupi lake kukhala limodzi ndi thupi la Muhammad.
Ndipo Mirza anati :
“ Allah anandipatsa udindo
wa Mtumiki oyela ndipo anandipangitsa mtima kwa Mtumiki wacifundo wa kuti ine
ndinakhala monga njira. Lero amene a tsata jamaat yanga akhala m’modzi wa
sahaba ya juma yanga yomwe inali kuposa Mtumiki onse. Sichili chinthu chobisika
kwa aja amene akwanitsa kuganiza kuti uku ndiko kutantha uza kwa mau asiyanitsa
ine ndi Mustapha (Mtumiki woyela pbuh) akalibe kundiona ndipo sandidzindikila.
(Khutbah-e-Ilhamjah,
Rohani Khazain, vol 16- pp.258-259)
kunali cabe kulindila
nthawi ndipo anayamba kunena kuti anabadwa kutenga mulo a Mtumiki woyela( SAW).
Lero GHULAM ANAKHALA MFUMU.
Mirza Ghulam Anena kuti
ndi Muhammad (SAW)
Mirza Ghulam akuti :
“Mtumiki woyela ali
kubwela kawiri kapena tingati kuti kubwela koyumba kunatsimikidzidwa ndi
kubwela kwa Messiah olengezedwa ndiponso Mahdi olengedzedwanso.”
(Roohan Khazain vol 17.
p.249)
Mirza Ghulam anati :
“ Ndakhala ndikunena
nthawi zambiri kuti kulingana ndi ndime (ya mu Qur’an oyela)”. Wa akhareena
minhum lamma yalhayoo behim’as Buwoz, nditi Mtumikii m’modzi-modzi, Khatamul
Ambiyyah ndipo zaka makumi awiri apitapo Mulungu anandipatsa dzina lakuti
Mohammed ndi Ahmad mu Baraheen-e-Ahmadiyya ndi kupanga ine kukhala iye.
(Aik ghalti ka azala,
Roohani Khazain vol 18 p.212).
Mirza Ghulam anati :
“Mtumiki oyela anabadwa kawiri monga Mtumiki. Mkunena kwina tingati kuti
chinalengedzedwa kuti Mtumiki woyela(SAW) adzakabadwanso mdziko ndiponso ichi
chinatsimidzedwa ndi kubadwanso kwa Messiah olenjedzedwa ndiponso Mahdi.
(Tohfa-e-Golrwia, Roohani
Khazain vo 17 p.249).
Mirza anati:
“ Pamene ndiri Mtumiki
woyela obadwanso kwa chiwiri, ndipo zonse pomwe zinacitidwa ndi Muhammad
kuonjezapo za utumiki, zioneka ngilasi kapena cilola changa, telo ndani wina
emwe anganena kuti ndi Mtumiki mwa iye yekha ?”
(Ek Ghalti ka Izala,
Roohani Khazain vol 18 p.212).
Zikhulupililo zotelezi ndi
zilembedwe za Mirza Ghulam Ahmad zinapangitsa kuti omutsatira ace kuti anene
mopanda manyazi zikhulupiliro zao.
Mirza Basheer Ahmad s/o
Mirza Ghulam a kuti: Maseeh Mawood salephera kulota ku Mtumiki woyela (pbuh),
koma ndi iye amene abwera ku chiwiri m’dziko monga Buroozi…lero kodi
palichikaiko ca kuti Mulungu watuma Mtumiki woyela kachiwiri ku Qadian ?
(Kalimat Alfasl p.104-105.
Review of Religions Qadian March 1915).
“Tsopano ndi chicodziwika
kuti kukana Mtumiki woyela ndi KUFR
ndiponso kukana Messiah olonjedzedwa ndiponso KUFR, chifukwa Messiah sasiyana
ndi Mtumiki woyela. Koma ndiye ngati iye
akana Messiah sali KAFIR terenso amene akuna Mtumiki woyelanso kafir, Mulungu aletsa.”
(Kalimat alFasl p.146-147.
Review of Religions Qadian, March- April 1915).
“Kodi kuli cikaiko cotsala
cakuti Mulungi watuma Mtumiki (pbuh) kwa chiwiri mu Qadian ku nsimikiza
chilonjezo?”
(Kalimat al Fasl by Mirza
Basheer Ahmad. Review of Religions p.105, N° 3
Vol 14).
Mirza alingana ndi Mtumiki
Woyela Muhammad
Inali njira ina yofuna ku
zilinganiza ndi Mtumiki woyera. Mirza
anati :
“Aliyense yemwe asiyanika
iye ndi MUSTAFA (pbuh) Sanandione ndipo Sandiziwa.”
(Roohani Khazain, vol 16 p.171)
Ololedwa kupambilako
Qadiani, Al-Fazl analemba kuti :
“ Chikhaliro cha
olengezedwa Maseeh (Mirza) nimaso mwa Allah ndi chikhaliro wa Mtumiki woyela
(SAW). Mchikumbukilo china,mzosungidwa za Allah kulibe kusiana pakati pa
Messiah olengezedwa ndi Mtumiki woyela (SAW). Koma onse agawana mpando olingana
ndipo ali ndi dziko limodzi. Angakhale kuti nimakambidwe ali awiri, awa ali
m’modzi ndipo olingana.”
(Al-Fazl, Qadiani, vol. N°
37 dated 1e September 1915,
as cited in Qadiani Muzhah page 207, ath edition-Lahore).
QADIANI KALIMA.
Mimalembedwa a oyamba
zinapangitsa nikhulupiliro izi :
“ Mkubwela kwa Messiah
olengezedwa, kusiyana kumodzi kwapezeka ndipo ndikwa kuti akalibe kubwela ka
chiwiri kwa Messiah olengezedwa, mcitanthauzilo kwa’Muhammadur RassuLullah’
Atumiki chabe amusiku akumbuyoku anali anaikidwapo, koma mkubwela kwa chiwiri
kwa Messiah olonyezedwa Mtumiki umodzi waonjezedwapo pa tanthauzo la Mohammadur
Resoolulah’…tero kumva mu Islam ndi kalima yemweyu, kusiyana kwekha komwe kulipo
ndi kwa kuti kubwela kwa chiwiri kwa Mtumiki kutanthauzo lache…sifuna kalima
watsopano, chifukwa Messiah wolonyezedwa sali opatuka kucokela kwa Mtumiki
woyela monga ali kunena ‘Saara wajuodi wajoodahoo (Manthu wanga anasanduka
munthu sanandine ndipo Sandizindikila’ … telo Messiah iye amene abwela ka
chiwiri m’dziko lino kuzafalitsa chi Islam, lero sitifuna kalima aliyense wa
tsopano ngati wina anabwela ndiye kuti
modzi tinafuna…telo onse muyenela kuganiza.”
(Kalimat Al-Fasl p. 158 na
Mirza Basheer Ahmad).
Chifukwa ca kubadwa kwa
Messiah tiolenjezedwa (Qadiani Mirza) kusiana kwabwela (mcitantha uzo ca
Kalimah). Akalibe kubadwa Messiah olonjezedwa (Qadian Mirza) m’dziko monga
Mtumiki, Mau akuti Muhammadur Rassolullah anaphatikiza mtanthauzo lawo, okhao
aporofeti omwe analiko iye akalike kubwela; koma pambuyo pobwelanso kwa Messiah
olonjezedwa (Qadiani Mirza) Kwa chiwiri m’maiko monga Mtumiki, Mtumiki umodzi
waonjezedwa ku tanthauzira la Muhammadur Rassoolullah. Lero mkulinganandi
kuukanso kwa Messiah olonjezedwa Kalimah, Mulungu akana, sikuthesedwa kuna
kuwala kuposa. Mwa chidule, Kalima ameneyu ali ndi mphawu m’mpingo tsopano
polowa MuchiIslam. Kusiyana kwache
kwa kukhalanso ndi thupi la Messiah
olenjezedwa (Mirza Qadiani) aonjezela Muhammadur Rasoolullah.” (Kalimatul Fasl
page 158, Mirza Bashim Ahmad Qadiani).
Kuonjezelapo, angakhali
kuti tivomera pakuganizira zomwe sizingacitike zakuti zina lolemekezedwa la
Mtumiki(pbuh). wolonjezedwa mu kalimah chifukwa cha kuti ye ndi othela wa
atumiki, angakhale lero palibe choipa ndipo sitifunanso Kalima watsopano
chifukwa cha kuti Messiah wolanjezedwa salipayekha kuchopa pa Mtumiki pakuti
iye (Mirza) yekha a kuti; “ Ine ndi chimodzi-modzi ndi Muhammadur Rasoolullah.”
Ndiponso “Iye amene a patula pakati pa ine ndi Mustafa Sandidziwa ndipo
Sandiona.”
Chomwe wamkulu Allah
analonjeza, cha kuti
azambwenzanso”Khatam-un-Nabiyeen m’dziko lino ka chiwiri monga
Mtumiki momwe olonjezedwa Mtumiki
Messiah (Mirza wa Qadiani) mwa iye Muhammadur Rasoolullah, amene anabwelenso
mdziko kaciwiri kumwaza uthenga wa Islam. Lero sitifuna Kalima watsopano.
QADIANI DUROOD SHAREEF
“ Lero mkulingana ndi
malembedwe a Qur’an, ‘anthu achikhulupiliro’ tumani Salaat yanu kwa iye ndipo
mulambile iye ndi ulemu (33:56) ndipo mkulingana ndi ma Hadiths amene muli
malamulo atumila Durod kwa Mtumiki woyela pbuh, kutuma Durood kwa Hazrat Maseeh
Dawood nkofunikila momwe muliri kofunikila kwa Mtumiki woyela pbuh.”
(Risala Durood
Shareef-Mohd Ismael Qadiani p.136).
Mkulingana ndi
zikhulupiliro za Islam ndi ma Hadith, nkojunikila kuonjezela M’baja lache
(Mtumiki woyela pbuh) mu Durood. Chimodzi-modzinso nkofunikila kutuma Durood
kwa Maseeh ndipo osakhala okhutila ndi Durood yomwe iya m’fikira iye (Mirza)
angakhalenso ngati wina watuma Durood kwa Mtumiki woyela pbuh. Telo Hazrat
Maseeh Mowood akuti :
“ Chimodzi pa zimene
zikanidwa ndi ayah amene (Mirza) agwilitsila kwa iye ma akuti ‘alaihe assalato
wa assalam ndipo kunena telo ndi HARAM. Yankho kwa ici ndilakuti ine ndine
Mtumiki wolonjezedwa, ndipo ndiika pambari zikambidwa za Salaat and Salaam,
Mtumiki woyela iye anati amene amupeza,
apeleka Salaam lache kwa iye ambiri, Salaam-o-Salaam yothokozera Messiah olonjezedwa.
Pamene mau otelewa okhuza
za amenewa ndi Mtumiki, sahabah anati,
Mulungu ndiye anati,lero chingakhale bwanji haram jama’at yanga kunena mau
otelewa kunenela ine.”
(Risala Durood Shareef,
Arba’een N° 2 Roohani Khazain vol. 17 p.349).
Mirza atengela
zilembedwa za Qur’an Loyela.
Uyu munthu ozinenela yekha
kuti akonda Mtumiki woyela mothelatu anayamba ziululidwa mwa woyela Mtumiki
Muhammad (SAW) kumuululika kuti zonse zolembedwa ziululidwa mwa Mirza Ghulam pa
ulemelelo wache.
Ngati mwatsegula mu
Haqeeqatul Wahy mu Volume 22 la Roohani Khazaini muzapeza kuti pa matsamba 77
kufikila tsamba 111. Mirza Ghulam anena za ziululidwe zace maka-maka mchitundu
cha Arabic. Omwe adziwa zilembedwe za Qur’an azadzindikila mwa muisanga za
kulengela kwa matembedwe a bukhuli. Mkati mwa zolembedwamo, muli ziululidwe
zomwe zinalembedwa kuthokoza woyela Mtumiki Muhammad ndi zina
zinagwilitsidwa Hazrat Ibrahim (AS). Ndi
dzitsanzo cabe zingono zomwe ziza kambidwa.
Allah athokoza Mtumiki
woyela Muhammad (pbuh) ndi anzake mu Qur’an loyela m’malembechwe awa :
“Muhammad Rasuulullah wal
ladhina m’ahuu, ashiddau’alal kuffur rahman bainahuù.”
Muhammad, mtumiki wa Allah
ndi aja omwe ali naye. (Al-Qur’an 8-29)
Mu zaka zikwi-zikwi zapita
kumbuyo uku, Ma Muslims sana khale ndi chitanthaulilo china cha verse kapena
zilembedwezi koma WAHI wa Mirza amvuza kuti :
“ Muhammad Rasoolullah wal
Ladhiina m’ahuu ashiddan’ala kuffaar whaman bainahum mchiutlidwe ici Mulungu
andipatsa dzina lakuti Mohammed ndipanso Mtumiki.” (Roohani Khazain vol 18
p.201)
Zotsatira ndi nindakaturo
za zilemedwe za Qur’an loyela zomwe ense mu Muslim okunda Mtumiki adzadzidzi
ndikala mwamsanga kuti athokoza Syedna Muhammad (SAW), zinaulidwanso kaciwili
kuthokoza Mirza Ghulam Atelo Mirza :
“ ‘Huwa Iladhi arsala
rasuulahu bil huda’ Iye mulungu neliye watuma mtumiki ndikumulangiza zacita.”
(al-Qur’an p:33)
“Subhana Ilahi asraa
bi’abdihii…alemekezedwe Allah amene anatenga kapolo wache usiku pa ulendo
wopita ku Masdjid AlHaram kupita ku Masjidal Aqsa…” (al-Qur’an 17:1)
“ Qul
in kuntum tuhibbunallaha fatabiun” akuti (O Muhammad) Ngati umukonda zoona
Allah, undilondele” (al-Qur’an 3:31)
“
Inna fatahua laka fata-han mubiina.” (al-Qur’an 48:12)
“ ‘Ya Siin walaalin Hakim.
Innaka la minal murSaliin… Yassen ! Zoona inu Muhammad muli m’modzi mwa
atumiki.” (al-Qur’an 36:1-3)
“ ‘Inna aatainaakal
Kawsar…’ Tamupatsaini inu mtsinje mu paradiso…” (al-Quran 108:1)
“ ‘Wa arsal naakal ila
rahmatan lil aalamiina.”
Ndiponso sitinakutume kuti
ukhale wachifundo kwa onse ni calo.” (al-Qur’an 21: 107)
Atatenga udindo wa woyela
Mtumiki (SAW), anayamba kudzipatsa iye tyekha uzidindo wina :
·
Mbanja lace linakhala AHLE BAIT
·
Anzake anakhala a Sahabah
·
Mkazi wace anakhala umm-ul-m’OMINEEN
·
Mosque yomwe inamangidwa ndi atate ace
inakhala al-AQSA MOSQUE QADIAN.
Kwa zaka zikwi-zikwi (1400
yrs) a Muslim sandziwa bwino za zobisika za dziko loyela la Jerusalem. Ndipo
mkulingana ndi Mirza Ghulam Masjid Aqsa, Qadian Mtumiki woyela anapita ku
Qadian osati ku Jerusalem pa usiku wa Ascension Mirza akuti :
“ Munalembedwe mu Qur’an
loyela (17:1) ‘Subhan alladhii asra bi’abdihii lailammin al Masdjid al Haram
ila al Masdjid alAqsa…’ Ulemu kwa iye amene anatenga kapolo wace usiku
kunicotsa kwa Masdjid Haram kumpereka kwa Masdjid Aqsa…Kutanthauza kuti Mosque
inamangidwa ndi atate ake a Mirza ndipo ku kulitsidwa kwace kwapangidwa ndi Mirza.”
Qadiyan inakhala
yocilizidwa monga ARDh-e-JARAM ndipo kuyendela malowa kunakhala cithoozi cha
Hajj:
“ Malo a Qadian ndi lemekezedwa. Khamu la anthu lalipanga
kukhala malo a Haram.” (Mirza Ghulam’s poetry Dur-e-Sameen p.58).
Anthu anapita ku superogatory
(Nafy) Hajj. Koma kumalowa (Jalsa Salama mu Qadian) ndipo lace ndilopambana
NAFIL HAJJ ndipo kusaikila nzelo sikwabwino pakuti njila yake (Ahmadiyya) ndi
yabwino ndipo zamtendere zichoka kwa Mulungu.
(Alna-e-Kamalat-e-Islam. Roohanni Khazain vo. 5- p.352)
Pakuti okhao amene ali
olemela ndiamene akwanitsa kupita ku Haji, osauka amewa lephela kupitako.Lero
Mulungu waikapa ZIL HAJJ kotelo kuti aja omwe ajuna kutukuta chikhulupililo cha
Islam ndi aja osauka a Muslim a ku India naonsO angapezekeko.” (Khutba Mlan
Mehmood Ahmad Khalifa Qadian, Pepala la Alfazl vol.20 N°66 lolembedwa pa 9 Dec.
1932).
Ndipo Pothela, koma osati
chothelelela, omwe anatenga mpando pambuyo pake anakhala “Khulafa-e-Rashideen.”
Pa nthawi Mirza anatha
matha ndipo anali kukamba momasuka za zikhulupiliro zace. Telo anaulula za WAHI
lake.
“ Chomwe chipangitsa
zikhulupililo zathu si Hadith ichi koma Qur’an ndi Wahi yomwe ibwela kwaine.
Inde, nikuonjezako tilangiza aja ma Hadith omwe ali nikulingana ndi Qur’an
ndipo satsutsana na WAHI langa. Ma Hadith ena, ndiataya kutali monga pepala
ilibe nchito.”
“ Mu Braheen-e-Ahmadiyya,
Mulungu aniitana nidzina la Ibrahimu.” (Arba’een n° 3. Roohan Khazain, vol 17
p. 420).
“Zophunzitsa zanga
ziphatikiza malamulo ndipo ziletsedwa ndi zifunilo za Shari’at. Pa chifukwa
ici, Mulungu apatsa dzina Wahi yanga ndi zomwe ndi chita lakuti ‘bwato’. Telo
unani ndi zikhulupiliro zanga ndi kuti ndine chombo cha Noah ndi
chopulumukilamo cha anthu onse. Lekani yemweali ndi matso aone ndipo amene ali
ndi matu anvele.” (Arba’een vol. 4 p.6 Roohani Khazain vol. 17 p.435).
“ Ndinena molumbila kwa
Mulungu kuti ndikhulupilila mu zomwe ndichita monga momwe ndikulupililanso
Qur’an ndi mabukhu ena a Mulungu. Monga momwe ndikhulupilila Qur’an mosakaika
kuti ndi bukhu la Mulungu, Chimodzi-modzinso ndikhulipilila kuti Wahi ija yomwe
itsika mwa ine ndi Mau a Mulungu. (Haqeeqat) Wahi Roohani Khazain vol 22 p.220)
“Chikhulupililo changa mu
Wahi chilingana ndi chikhulupililo comwe ndili nacho mu Qur’an ndi Torah.”
(Haqeeqatul Wahi, Roohani Khazain vol.22 p.401)
Mirza ndiopambana pa
Mtumiki woyela Muhammad SAW (ma’azAllah):
Mirza Ghulam Ahmad anali
akali osakhutila. Anali kufuna kupitililapo. Chomwe anacita cholondolapo
chinali chozikutitsa kupambana Mtumiki woyela Muhammad (SAW). Ndipo anati :
“ Koma ceni-ceni ndi ca
kuti za uzimu za Mtumiki woyela pbuh
(mwa Mirza Ghulam) Kuthela malemba ya chisanu ndi kamodzi, ndi zamphamvu
kwambiri mkulinganiza ndi zaka zakumbuyoku. (Khutba-e-Illhamiah, Roohani
Khazain vol.16 p.271)
Za nzimu za mporofeti
wathu oyela (SAW) zinali zobisiku mu 5th thousand (Makk’i birth)
ndipo nthawiyi sinali yapamwamba mkukula kwa zauzimuwace. Koma uku kunali
koyambilila kufika pa mwamba-mwamba pa tsanja ya zabwino. Pambuyo pace, za
uzimuzi zinafika pa chimake mu 6 th thousand (Kubadwanso kwace mu
Qadian) pa nthawi imeneyi. (Mirza in Khutba-e- Ilhamiyah, Roohani Khazain vol.
16 p.266).
Anthu omwe anali kumtsata
anawauza kuti anapatsidwa zi zindikilo ndi zodabwitsa zokwanila 300 000 pamene
Mtumiki woyela anapatsidwa cabe 3000. Mozikuza yekha, analemba kuti : “Kwa
Mtumiki woyela, Mulungu anamuonetsa cabe eclipse ya Mwezi. Koma ine anionetsa
Ma Eclipse yonseya Mwezi ndiponso ya dzuwa, lero kodi
simudzandikhululupililila?” (Aijaz-e-Ahmadi, Roohani Khazain vol.19 p.183)
Ananena kuti zambiri
zobisika za mu Qur’an kapena zinanthauzo za cinsinsi sizinachulidwe kwa Mtumiki
woyela (SAW) koma iye wauzidwa pa izi. Tele Mtumiki woyela sanadziwe tauthauzo
la Ibne Maryam, Dajjah, Donkey dajjah, Gog ndi Magog, Daabah) Ardh.
(Izala-e-Auham, Roohani Khazain vol 3 p.473).
“Uisilamu wa Mtumiki
woyela unaoneka ngati Mwezi wa tsopano
(Mthawi ya Mirza) ndipo unali kuyembekezedwa kasanduka monga mwezi odzala.”
(Roohani Khazain vol 16 p.184)
“ Nchodziwikilatu kuti
Fath-e-Mubeen anabwela pa nthawi ya Mtumiki wathu ndipo kupambana kwima
kunatsala komwe kuli kwa kukulu ndi kodziwikilato ndipo nthawi yace ndi nthawi
ya Messiah wolonjezedwa.” (Roohani Khazain vol.16 p.288).
Chinenedwe ici cinanenedwa
pamatso pa Mirza ndi anthu omwe anali kunitsata. Kwanenedwa kuti Mirza anati :
Jazakallah ndipo atalemba malembedwe a bwino, anapachika zolembedwazi m’nyumba
yace.
“ Muhammad watsikanso pa
ife ndipo ndiochuka kuposa kale. Amene afuna ku muona iye bwino-bwino ayenera
kuyangana Ghulam Ahmad mu Qadiyan;.” (Qazi Zahoor Ahmad Akmal Qadiani
yolembedwa mu pepala la Paigham-us Sulh- 14th March, 1916).
“ Kukula kwa nzeru kwa
Messiah wolonjezedwa (Mirza of Qadian) ndi kupambana Mtumiki woyela (pbuh). Iyi
ndi mbali cabe ya kukula kwa Messiah wolonjezedwa kuposa Mtumiki woyela.”
Mirza apatiliza
kumcepetsa Mtumiki oyela Muhammad (SAW).
Mtumiki woyela sanadziwe
tanthauzo la Surah Azilzal (Roohani Khazain Vol 3, pp;166-167)
Zomwe anaulula Mtumiki
woyela zinasanduka zaboza. (Roohan Khazain Vo l3 p.472)
Mtumiki oyela analakwa
mkumvetsa kwa zouliludwa (Roohani Khazain Vol 2 p.224).
Manda a Mtumiki woyela ndi
malo oyopedwa kwambiri ndi a Muslim dziko lonse.
“Lero Mulungu anatsankha
malowa kuti aikepo Mtumiki woyela (pbuh)
omwe anali oipa ndipo onunkha kwambiri ndiponso
wamdima, malo umwe anali odzala ndi matubvi atidoyo…” (Roohani Khazain
Vol 17 p.205).
Akuzipanga kuti
ndiye Mtumiki othela.
Pa nthawiya, Sichinali
choodabwitsa kuti anali kunena kuti ndi Mtumiki othela.
“ Mwa nthawi zambiri
ndakhala ndiri kunena kuti nikulingana ndi verse, ‘Wa aakhareena minhuru lamma
yalhaguo belim-ndi ena omwe akalibe kuzionjezela pa iwo…’ (al-Qur’an 62:3) mu
BUROOZI, halili Mtumiki m’modzi-mdozi KHATUM-UL-ANBIYA (othera wa Atumiki). Zaka
makumi awiri apita kumbuyoku Mululngu ananicha Muhammad ndi Ahmad mu
Braheen-e-Ahmadiyya ndikunena kuti ndine Mtumiki woyela (pbuh) omwe atenga nalo
a Mtumiki emwe analipo. Lero Utumiki wanga siutsutsana ndi Utumiki wa Mtumiki
woyela (pbuh) wanga Mtumiki wothela
chifukwa cha kuti nkosatheka kupatula cithunzi, kuchoka ku chinthu chomwe
chapanga chithunzico pakuti ndi chinthunzice cha Muhammad, lero ndiri Mtumiki
wotsiriza pakuti Utumiki wa Muhammad
unatsala ndi Muhammad.” (Mirza Ghulam in Ghalti ka Izala, Roohani Khazain vol 8
p.212 ).
“ Niodala iyo amene
andidziwa . Pa njila zonse zopita kwa Mulungu ine ndine njile yothela, ndipo pa
zowala zace, ine ndine njila yothela, ndipo pa zowala zace, ine ndine kuwala
kokhela. Koma tsoka kwa iye amene satsata ine cifukwa chakuti popanda ine,
zonse zili munidima.” (Kashti-e-Nooh, Roohani Khazain vol 19 p.61 ).
“ Ndine ndekha demwe
wasankhidwa mu Ummah kutenga dzina la mtumiki.” Palibe wina aliyense amene
angapatsidwe dzinari…ndipo dzinari kufuna kuchitidwa…monga momwe zinanenedwa mu
Sahihi Hadith kuti kuzakhala cake munthu ekhayo nimodzi ndipo chinenedwechi chatsimikizidwa.” (Haqiqeetul
Wahy; Roohani Khazain Vol 22 p.401).
Umtumiki unathela pali
mtumiki wathu (pbuh). Lero mpambuyo pace palibe Mtumiki wina
kuchotsako yemwe wakudziwa ndi kuwala kwace ndipo wapangidwa kutenga
inalo ace ndi Mulungu. Dziwani kuti kumathelo kunapatsidwa kwa Muhammad (pbuh)
kucoka pa chiyambi ndiku patsidwa kwa
iye (Mirza) amene anaphunzitsidwa ndi uzimu wace ndikumupa chithunzi cace. Lero
diodala amene aphunzitsa ndiponso
ndiodalanso amene amphunzira (Mirza) . Lero Mthero anaikidwa mu
Malembamu ya chisanu ndi kamodzi.
(Zamima Khutba Ilhamiah, Roohani Khazain vol 16 p.310).
Mirza BasheerAhmad s/o
Mirza Ghulam analemba kuti:
“ Lero munthu m’modzi
yekha anatenga udindo wa Utumiki mu Ummah wa Muhammad… kucotsako cabe Messiah
walonjedzedwa (Mirza) kulibe wina analondola Mtumiki woyela. Motelo, ndi Messiah olonjezedwa cube
amene anasankhidwa kuchedwa mporofeti.” (Kalimat Al-Fast, Review of Religions,
Qadian p.116 N° 3).
Magazini yololedwayo
Qadiani analemba kuti :
“ izi zolembedwa zionetsa kuti ndi Messiah cabe wolonjezedwa
amene angakhale Mtumiki… Pambuyo pa mporofeti oyela (pbuh) Mtumiki nimodzi cabe
anali kufumka ndipo kubwela kwa a Mtumiki ambiri kunakazokoneza zifunilo za
Mulungu ndi zomwe anali kufuna kucita.” (Tasheed-ul-azhan, Qadian, n° 8, vol 12,
pp.11, August 1917).
CHI ISLAM
CHOMWE CHINALIKO MIRZA
AKALIBE KUBWELA NDI CHI
ISLAM CHAKUFA
Maka-maka mu chaka cha 1906, mwa maganizodwe a Khwuja maluddin, Moulvi Muhammad Ali analowa
nchigwilizano ndi mkulu wa Akbar-e-Watan (wowona pa zilembedwe) kuti aone kuti
zolembedwa zao siziulutsa za cikhulupililo ca ka guru ka Qadiani. Zolembedwa
zinali kufunika chabe kuulutsa za cikhulupiliro cha Islam. Olonjezedwa Maseeh
anakana zamaganizo awandiponso a Jamaat naonso, Hazrat Sahib anati.”
“ Muzanena za Islam mu
dziko mosandiikako ine?.” (Zikr-e-Habib by Mufti Muhammad Sadiq Qadian p.146.
First Edition).
“ Tikhulupilila kuti
mpingo yomwe alibe chiphupirio cha Utumiki (Monga mu Islam) ndi mpingo yakufa.
Tunanena ma religion ene monga ma Yahudi, ma christu ndi ma Hindus kuti ndi m’mpingo yakufa
chifukwa cha kuti alibe Mtumiki .Kodi nchifukwa ninji tinena kuti Islam
ndiyopamnana pa m’mpingo ena onse ?” Iyenela kuti isiyane.” (Malfoozat-e-Mirza,
Vol.10 p.127).
MIRZA ANENA KUTI ISLAM NDI
YACABE-CABE NDIPO NDI YA USATANA
“ Kuti mpingo si mpingo
ndi Utumiki si Utumiki pakulondola munthu amene salipafupi ndi Mulungu kuti
apatsidwe mphamvu zace. Kuti mpingo ndiwa chabe-cabe yomwe uphunzitsa anthu
kuti chitukuko cha munthu chiyembedwa cabe pa zomwe zilembedwa mu Qur’an loyela
ndi mu Shari’at-e-Muhammadia yomwe inanenedwa ndi Mtumiki woyela (pbuh) ndipo
kuti ‘WAHI’ yatsata mu mbuyo m’malo mopita pa tsogoro… lero chimpingo
chotere chiyenekela kuchedwa kuti ndi
chansatana osati cha Mulungu. (Zamima
Braheen-e-Ahmadiyya, part V. Roohani
Khazain Vol 21 p.306).
“ Ndi chodabwitsa
kukhulupilila kuti pambuyo pa Mtumiki woyela (pbuh) Chitseko cha ‘wahi’
chatsekedwa ndipo kulikenso chiyesezelo chanaco mpaka tsiku loika-lamba cabe .
Kuli mpingo yomwe sikhuzana ndi wamkulu Allah yomwe ingachedwe mpingo ?…
ndinena mwa Mulungu wamkulu, kuti nimasiko ano, kulibe amene ati nkhidwa kopambana
ine mu mpingo yotere. Ndinena mpingo wotereyi
ndiusatana ndipo kuti
mpingo ya jehena
ya kumoto ndikutseka maso a
munthu mpaka kufu kwache.” (Zamina Braheen-e-Ahmadiyya part V).
MIRZA NDI QURAN YOYELA.
“ Qur’an ndi bukhu la
Mulungu ndi mau amukamwa mwanga.” (Adversement dated 15th March
1897, Roohani Khazain vol 22 p.87).
pamene Mirza Ghulam Ahmad
anaudzidwa kuti zolembedwa zace zinyoza aja amene anali kutsutsana naye, anane
kuti Qur’an nayonso ili ndimau ambii vipa ndipo anafotokoza kuti sanali
kufikako pa zofunikila za masiku ano. (Roohani Khazain Vol 3 p.115-117 ).
ZOSINTHIDWA MU
QUR’AN YOYELA
Pali njira zambiri zomwe
izi zingantidwe:
Kusintha kwa mau
Kusintha kwa zitanthauzo
Kusintha kwa zindime
Kucotsa zikakamizo za Qur’an
Mirza Ghulam Ahmad
anapezeka ndi milandu yonse inai. Angakhale kuti sanasithe ziri zonse
zolembedwa mu Arabic m’bukhu la Qur’an, koma m’malembedwa ace ocotsa mbukuli,
asintha mwadala zina zolembedwa mwa Arabic. Zitsanzo za zina za lembedwa mu
matsamba otsatila.
Chitsanzo chodziwika
kwambiri pa zosinthidwa za matanthauzo a Qur’an loyela ndi ndime la 3 :
144 lomwe linene pa KUTHA KWA UTUMIKI
Kuchoka pa chiyambi cha
Islam, pa nthawi ya Mtumiki woyela
Muhammad kufikira lero lino, onse ma Muslims anaciona chinthu chosasokoneza pa
MirzaGhulam Ahmad yemwe mu zaka zoyambilira anali ndi chikhulupiliro chotere.
Koma pambuyo pace pomwe maganizo ace anasintha, anapatsa chinenero chotere cha
kuti Utumiki wa Muhammad siunathero koma masegulidwe a Mtumiki amtsogolo, Monga
kuti ALLAH, yemwe anatumiza Atumiki
124.000 la amupatsa udindo Mtumiki woyela Muhammad. Atero anena kuti ndiye
adzakhala Mtumiki wotsatiripo, kuunika kokhera pakati pa kuunika konse kwa
Allah. M’manenedwe ena, zonse zokambidwa zosokoneza mitu zomwe anapatsa
m’mabukhu ache mu ndime imeneyi zinali zofuna cabe kupititsa pa tsogolo Utumiki
wace. Atsegula chitseko cha KHATME NABUWWAT, alowa ndiponso atsekanso. Kodi
sichitsanzo cha chikuri chakuba chimeneci ?
Chimodzi-modzi owelenga
zoleyembedwa kuti anawelenga momwe ndime
zotamanda Mtumiki woyera Muhammad SAW
zinasinthidwa ndi Mirza.
Kulakwira kwa JEHAD ndi
Mirza Ghulam Ahmad ndi chitsanzo chutuma kuyesa malamuro a Qur’an.
Tingagwiritse nchito chilembedwe Chimodzi.
“ Kucoka lero jehadi ya
munthu yomwe icitidwa ndi panga, linakwilidwa ndi kulamulidwa kwa Mulungu.
Kuyambila lero, aliyense amene anyamula panga kunyamulura kaafir ndi kuziyitana
iye kuti ndi GHAZI ali ku lakwira otumidwayo (SAW), amene ananena kwa zaka 1300
zapita kumbuyo kuti pambuyo pobwela
Messiah olenjezedwa onse ma jehads ali ndi ma panga azatha. Telo pakubwela
kwanga KULIBE JEHAD ALIYENSE AMENE ALI NDI PANGA. (Collection of Advertisement
p.295, vol.3 ).
“ Kochoka pomwe ndinali
mwana kufikila lero pomwe ndiri ndi zaka 65, ndakhara ndiri kugwira nchito ya
cholembetsa ndi lirime langa pakufuna kusintha m’tima ya ma Muslim’s kuti
akhale a chikondi, a chikhulupiliro ndi a chifundo kwa boma la British
ndikucotsa ganizo la jehad m’mtima ya Aslims opusa.” (Kitab-ul-Bariya, (Roohani
Khazain Vol 13 p.350).
“…Mmalo Boma la
Azungu (British) ndaulitsa ndikufalitsa timapepala 50,000 mdziko lino
(India) ndi maiko ena a chi Islam kudzudzula Jehadi…zokoma zake ndi zakuti
anthu masauzande ambiri asiya maganizo ao oipa a jihad.” (Roohani Khazain Vol
15 p.114).
Munthu wina anafunsa funso
pa za ma Muslims ndipo Mirza anayankha motere ndipo yankhoyi ifunika ku
welenga. Zonse ziwiri zinalembedwa mu bukhu lache, Haqeeqat-up-Wahy:
“Funso : Huzoor-e-aali
anena mmaro ambiri-mbiri uti sichili chofunika kuyitana KAFIR kuti Kalima-jo
(Mnthu amene anayeselela Kalima) ndiponso Ahle-Qibla. Ndi chodziwikilatu kuti muchitsazo chi, Momineen amene anakhala
Kafir pokukana, koposa kumvomelera iye, palibe amene akhala Kafir. Koma mulembe
kwa Abdul Hakeem Khan kuti aliyense amene alandila uthenga wanga.
Koma sanandikolole kapena
kundivomela ine, iye Muslim. Kuli kutsutsana pa mava awa ndi mau omwe
analembedwa kumbuyoku. Poyambilira mu Tiryaqul-Quloob munanena kuti palibe
amene akhara Kafir posakukumbukirani koma tsono mulemba kuti pa kukana inu, iye
akhala Kafir.
Yankho: Ndi chodabwitsa
kuti mpinga munthu amene akana ine ndi munthu amene iatana ine kuti Kafir ndi anthu osiyana, pomwe mmaso mwa Mulungu
ndi munthu m’modzi; chifukwa amene akana ine chifukwa cha kuti azonda ine. Mingu Munthu
wabodza-kuchotsako ichi, iye amene sandilora sakhulupirira mwa Mulungu ndiponso
mwa Mtumiki. (Haqeeqat-ul-Wahy, Roohani Khazain Vol 22 p.167).
“Kuchotsako ANA ANTHU
ACHIWERE-WERE, omwe mitima yao ndi yotsekedwa ndi Mulungu, aliyense
akhulupilila mwa ine. (Aina-e-Kamalat-e-Islam, Roohani Khazain Vol 5 p.547).
“Mulungu a ndiuza kuti ali yense emwe walandira uthenga wanga
ndipo sanandimvomera, ameneyu sali mu Muslim. (Kalata ya Mirza kwa Dr Abdul
Hakeem Khan Patialvi)
“Ndiri ndi chifuniro cha
Mulungu cakuti iye amene sakulondola ndiponso sazalowa mu B’ith yako ndikukhala
otsutsana ndi iwe kapena mdani wako, alibe ulemu kwa Mulungu ndi kwa Mtumiki,
Hellish;” (Advertisement mu M’ayaar-ul-Akhyarya Mirza Ghulam p.8)
“Lero kumbukirani momwe
Mulungu andiuzila kuti ndi chosaroredwa kupemphelera kumbuyo kwa emwe
sakhulupilila ndiosafuna, koma kuti Imam yako akhale umodzi wa iwo.” (Arbaeen
n° 3, Roohani Khazain vol 17 p.147 just note).
MATHERO
Kwa Owelenga!
Ndikhulupilira pa nthawi
ino mwaona chomwe munthuyu anali kulingalira. Kudzionetsa kwa kuti anali ndi
chikondi cha chikuri cha Utumiki wa UIslam kunali kudziwa lingo lache kuti
atsate guru la Ahmadiyyah. Mafunso omwe muyenera kuzifunsa inu nokha ndi aya;
Kodi zilembedwe za
m’bukhuri ndizoona ?
Ngati ndizoona, nanga
Mirza Ghulam Ahmad, amene anayamba Ahmadiyyah
anamuyamika mwachoonadi Syedna Muhammad kapena anamunyoza?
Kodi munthu woteleyo ndi
olongosoka ?
Ngati nitelo, kodi munthu
oteleyi tinganene kuti ndi mu Muslim ?
Nanga nchiani chomwe
chipangitsa agulu la Ahmadiyya kubisa
izi zokhuzana ndi munthu amene anayamba gururi ?
Kodi Ahmad ndiolondola
weni-weni wa Mtumiki woyela SAW ?
Kodi ameneyu anali munthu
otani ?
Angakhale ziganizo zanu
zikhale zotani, Mirza Ghulam Ahmad iye izinena motele:
Ndiri unyolo mzanga !
Osati munthu, ndili mbali yosaoneka ya munthu ndi malo mvetsa manyazi ku anthu.
(Tanthauzo La mau mu Urdu ndi malo yabisika ya anthu olemba)
(Braheen-e-Ahmadiyya V,
Roohani Khazain vol 21 p.127 ).
Tipempha Allah aonetsa
kuwara kwa Islam ku onse omwe anasochela chifukwa cha zi chilidwe zotelezi mu
dzina la Islam. Allah achinjilize chikhulupililo cha ma Muslims onse ku zoipa
zoterezi.
Ameen.
Mtendele ukhale kwa iwo amene olondora
njira yoona.
ANTI AHMADIYYA MOVEMENT
IN ISLAM
SYED ABDUL HAFEEZ
SHAH
DR SYED RASHID ALI
P.O BOX 11560
Dibba Al Fujairah
United Arab
Emirates
Fax (9719) 442846